13. Pamene Efraimu anaona nthenda yace, ndi Yuda bala lace, Efraimu anamuka kwa Asuri, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuciritsani, kapena kupoletsa bala lanu.
14. Pakuti ndidzakhala kwa Efraimu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kucoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.
15. Ndidzamuka ndi kubwerera kumka kumalo kwanga, mpaka adzabvomereza kuparamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwacangu.