1. Imvani mau a Yehova, inu ana a Israyeli; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe coonadi, kapena cifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.
2. Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kucita cigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.
3. Cifukwa cace dziko lidzacita cisoni, ndi ali yense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzacotsedwa.