Hoseya 11:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.

10. Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.

11. Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Aigupto, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asuri; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova.

Hoseya 11