Habakuku 2:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wocurukitsa zimene siziri zace! mpaka liti? iye wodzisenzera zigwiriro.

7. Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?

8. Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.

9. Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yace phindu loipa, kuti aike cisanja cace ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la coipa!

10. Wapangira nyumba yako camanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wacimwira moyo wako.

11. Pakuti mwala wa m'khoma upfuula, ndi mtanda wa kuphaso udzaubvomereza.

12. Tsoka tye wakumanga mudzindi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi cisalungamo!

13. Taonani, sicicokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto nchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pace?

Habakuku 2