Genesis 8:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la cingalawa limene analipanga:

7. ndipo anaturutsa khungubwe, ndipo anaturuka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi,

8. Ndipo anaturutsa njiwa imcokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi;

9. koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lace, nibwera kwa iye kucingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anaturutsa dzanja lace, naitenga, nailowetsa kwa iye m'cingalawamo.

10. Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; naturutsanso njiwayo m'cingalawamo;

11. ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwace munali tsamba lazitona lotyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi.

12. Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; naturutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye.

13. Ndipo panali caka ca mazana asanu ndi limodzi kudza cimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anacotsa cindwi lace pacingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi.

14. Mwezi waciwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi.

Genesis 8