1. Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m'cingalawamo; cifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.
2. Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yace; ndi nyama zosadyedwa ziwiri ziwiri yamphongo ndi yaikazi yace.