Genesis 49:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Dani adzakhala njoka m'khwalala,Songo panjira,Imene iluma zitende za kavalo,Kuti womkwera wace agwe cambuyo.

18. Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.

19. Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.

20. Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.

21. Nafitali ndi nswala yomasuka;Apatsa mau abwino.

22. Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.

23. Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza:

24. Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)

25. Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.

26. Madalitso a atate wakoApambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire;Adzakhala pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.

27. Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;M'mamawa adzadya comotola,Madzulo adzagawa zofunkha.

28. Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wace anawadalitsa.

29. Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga liri m'munda wa Efroni Mhiti,

Genesis 49