Genesis 45:26-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Aigupto, Pamenepo mtima wace unakomoka, pakuti sanawakhulupirira iwo.

27. Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magareta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

28. ndipo Israyeli anati, Cakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.

Genesis 45