Genesis 41:52-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. Ndipo dzina la waciwiri anamucha Efraimu: cifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.

53. Ndipo zaka zakucuruka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Aigupto, zinatha.

54. Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Aigupto munali cakudya.

Genesis 41