22. Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu: mlongo wace wa Lotani anali Timna.
23. Ana a Sobali ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebali, Sefo ndi Onamu.
24. Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.
25. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.
26. Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana.
27. Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani.
28. Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana.