Genesis 36:21-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. ndi Disoni ndi Ezeri ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m'dziko la Edomu.

22. Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu: mlongo wace wa Lotani anali Timna.

23. Ana a Sobali ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebali, Sefo ndi Onamu.

24. Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.

25. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26. Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana.

27. Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani.

28. Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana.

Genesis 36