7. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, Dacha pamenepo El Beteli: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wace.
8. Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Beteli, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anacha dzina lace AlioniBakuti.
9. Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anacokera m'Padanaramu, namdalitsa iye.
10. Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israyeli: ndipo anamucha dzina lace Israyeli.
11. Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, ucuruke; mwa iwe mudzaturuka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzaturuka m'cuuno mwako;
12. ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isake ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.