29. Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina cifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
30. Ndipo anacha dzina la malo amenewo, Penieli: cifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga,
31. Ndipo kudamcera iye pamene analoloka pa Penieli, ndipo iye anatsimphina ndi ncafu yace.
32. Cifukwa cace ana a Israyeli samadya ntsempha ya thako iri pa nsukunyu ya ncafu kufikira lero: cifukwa anakhudza nsukunyu ya ncafu ya Yakobo pa ntsempha ya thako.