Genesis 27:13-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo amace anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.

14. Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amace; amace ndipo anakonza cakudya cokolera conga cimene anacikonda atate wace.

15. Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;

Genesis 27