4. Ndipo Abrahamu anamdula mwana wace wamwamuna Isake pamene anali wa masiku ace asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye.
5. Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isake mwana wace.
6. Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.
7. Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wace.