Genesis 13:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema.

6. Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: cifukwa kuti cuma cao cinali cambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

7. Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperezi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.

8. Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisacite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: cifukwa kuti ife ndife abale.

9. Dziko lonse siliri pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.

10. Ndipo Loti anatukula maso ace nayang'ana cigwa conse ca Yordano kuti conseco cinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakunka ku Zoari.

11. Ndipo Loti anasankha cigwa conse ca Yordano; ndipo Loti anacoka ulendo wace kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzace.

Genesis 13