6. Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali naco cinenedwe cao cimodzi; ndipo ici ayamba kucita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kucita.
7. Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze cinenedwe cao, kuti wina asamvere cinenedwe ca mnzace.
8. Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi.
9. Cifukwa cace anacha dzina lace Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza cinenedwe ca dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.