Ezekieli 48:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo madera otsalawo m'litali mwace alingane ndi copereka copatulika, ndico zikwi khumi kum'mawa, ndi zikwi khumi kumadzulo, alingane ndi copereka copatulika; ndi zipatso zace zikhale za cakudya ca iwo ogwira nchito m'mudzi.

19. Iwo ogwira nchito m'mudzi mwa mafuko onse a Israyeli alimeko.

20. Copereka conse ndico mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace; mucipereke copereka copatulika camphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.

21. Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali yina ndi yina ya copereka copatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu za copereka ku malire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu ku malire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo ca kalonga; ndipo copereka copatulika ndi malo opatulika a kacisi zidzakhala pakati pace.

22. Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ace a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.

23. Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikita mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi.

24. Ndi ku malire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.

25. Ndi ku malire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.

26. Ndi ku malire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.

27. Ndi ku malire a Zebuloni, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.

28. Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwela, kuloza kumwela, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati ndi Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, kufikira ku nyanja yaikuru.

Ezekieli 48