1. Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa ciundo ca nyumba kum'mawa; pakuti khomo lace la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kucokera pansi pa nyumba, ku mbali ya lamanja lace, kumwela kwa guwa la nsembe.
2. Pamenepo anaturuka nane njira ya ku cipata ca kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kumka ku cipata cakunja, njira ya ku cipata coloza kum'mawa; ndipo taonani, panaturuka madzi pa mbali ya kulamanja.
3. Poturuka munthuyu kumka kum'mawa ndi cingwe coyesera m'dzanja lace, anayesa mikono cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo.
4. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'cuuno.