Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.