Ezekieli 40:32-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa cipata ca kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;

33. ndi zipindazace, ndi makhoma a pakati pace, Indi zikundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

34. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.

35. Pamenepo anabwera nane ku cipata ca kumpoto, naciyesa monga mwa miyeso yomweyi;

36. zipinda zace, makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

Ezekieli 40