Ezekieli 34:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nkhosa zanga zinasokera ku mapiri ali onse, ndi pa citunda ciri conse cacitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.

7. Cifukwa cace abusa inu, imvani mau a Yehova:

8. Pali ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala cakudya ca zirombo zonse za kuthengo, cifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafuna nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;

9. cifukwa cace, abusa inu, imvani mau a Yehova:

Ezekieli 34