13. Ndipo ndidzaziturutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israyeli, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.
14. Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri atali a Israyeli padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsetsa pa mapiri a Israyeli.
15. Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.
16. Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yotyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo; koma yanenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi ciweruzo.
17. Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.