Ezekieli 33:28-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israyeli adzakhala acipululu, osapitako munthu.

29. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, cifukwa ca zonyansa zao zonse anazicita.

30. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe ku makoma ndi ku makomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wace, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.

31. Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawacita; pakuti pakamwa pao anena mwacikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.

Ezekieli 33