10. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wace, nufikitsa nsonga yace kumitambo, nukwezeka mtima wace m'kukula kwace,
11. ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzacita naotu, Ine ndautaya mwa coipa cace.
12. Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zace zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zace zinatyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika ku mthunzi wace, niusiya.
13. Pogwera pace padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zace;
14. kuti mitengo iri yonse ya kumadzi isadzikuze cifukwa ca msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa ku imfa munsi mwace mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.