Ezekieli 31:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi wacitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aigupto ndi aunyinji ace, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?

3. Taona, Asuri anali mkungudza wa ku Lebano ndi nthambi zokoma zobvalira, wautali msinkhu, kunsonga kwace ndi kumitambo.

4. Madzi anaumeretsa, cigumula cinaukulitsa, mitsinje yace inayenda, nizungulira munda wace, nipititsa micera yace ku mitengo yonse ya kuthengoko.

Ezekieli 31