Ezekieli 24:25-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwacotsera mphamvu yao, cimwemwe cao copambana, cowakonda m'maso mwao, ndi cokhumbitsa mtima wao, ana ao amuna ndi akazi,

26. kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m'makutu mwako?

27. Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso cete, momwemo udzawakhalira cizindikilo; ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.

Ezekieli 24