28. Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pace, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova posanena Yehova.
29. Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwaciwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda cifukwa.
30. Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.
31. Cifukwa cace ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yao yao ndinaibweza pa mutu pao, ati Ambuye Yehova.