Ezekieli 21:31-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.

32. Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndacinena.

Ezekieli 21