Ndipo kunali caka cacisanu ndi ciwiri, mwezi wacisanu; tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israyeli kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.