4. Mitundu ya anthu idamva mbiri yace, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera ku dziko la Aigupto.
5. Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti ciyembekezo cace cidatha, unatenga wina wa ana ace, numsandutsa msona.
6. Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.
7. Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwace linasanduka labwinja, cifukwa ca phokoso la kubangula kwace.