14. Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zocimwa zonse adazicita atate wace, naopa wosacita zoterezo,
15. wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace,
16. kapena kusautsa wina ali yense, wosatenga cigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,
17. naletsa dzanja lace pa wozunzika, wosalandira phindu kapena coonjezerapo, wocita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wace, adzakhala ndi moyo ndithu.
18. Atate wace, popeza anazunza cizunzire, nafunkha za mbale wace, nacita cimene siciri cabwino pakati pa anthu ace, taona, adzafa mu mphulupulu yace.