12. Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Liri kuti dothi munalimata nalo?
13. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.
14. M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ace agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pace; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
15. M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,
16. ndiwo aneneri a Israyeli akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.