Ezekieli 10:21-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi cifaniziro ca manja a munthu pansi pa mapiko ao.

22. Ndi cifaniziro ca nkhope zao ndico nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; ali yense anayenda, nalunjika m'tsogolo.

Ezekieli 10