7. Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
8. Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.
9. Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.
10. Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.
11. Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.
12. Ndipo zinayenda, ciri conse cinalunjika kutsogolo kwace uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.
13. Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.
14. Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.
15. Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16. Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.