Ezara 2:40-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyeli, ndiwo a ana a Hodariya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.

41. Oyimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

42. Ana a odikira: ana a Sabumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai.

43. Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

44. ana a Kerosi, ana a Siaha, ana a Padoni,

45. ana a Lebano, ana a Hagaba, ana a Akubu,

46. ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani,

Ezara 2