1. Zitatha izi, mfumu Ahaswero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wace upose akalonga onse okhala naye.
2. Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'cipata ca mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira cotero za iye. Koma Moredekai sanamweramira kapena kumgwadira.
3. Ndipo anyamata a mfumu okhala m'cipata ca mfumu anati kwa Moredekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu?
4. Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Moredekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda.