15. Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonoogeke pa dziko lapansi.
16. Koma ndithu cifukwa cace ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.
17. Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?
18. Taona, mawa monga nthawi yino ndidzabvumbitsa mbvumbi wa matalala, sipadakhala unzace m'Aigupto kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
19. Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.
20. Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ace ndi zoweta zace;
21. koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zace kubusa.
22. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Aigupto, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Aigupto.