5. Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao,
6. Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,
7. Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.
8. Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musacepsapo, popeza acita cilezi; cifukwa cace alikupfuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.