Eksodo 5:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo mfumu ya Aigupto inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, cifukwa ninji mumasulira anthu nchito zao? Mukani ku akatundu anu.

5. Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao,

6. Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,

7. Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.

8. Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musacepsapo, popeza acita cilezi; cifukwa cace alikupfuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.

9. Ilimbike nchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.

10. Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anaturuka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.

Eksodo 5