13. Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani nchito zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace, monga muja munali ndi udzu.
14. Ndipo anapanda akapitao a ana a Israyeli, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji nchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?
15. Pamenepo akapitao a ana a Israyeli anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu?
16. Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.
17. Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: cifukwa cace mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.