11. Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzacepa pa nchito yanu.
12. Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Aigupto kufuna ciputu ngati udzu.
13. Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani nchito zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace, monga muja munali ndi udzu.
14. Ndipo anapanda akapitao a ana a Israyeli, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji nchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?