22. Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova, Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israyeli.
23. Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
24. Ndipo kunali panjira, kucigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.
25. Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo iye anamleka.
26. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, cifukwa ca mdulidwe.
27. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kucipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona.
28. Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikilo zonse zimene adamlamulira.
29. Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akuru onse a ana a Israyeli;