Eksodo 29:29-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo zobvala zopatulika za Aroni zikhale za ana ace amuna pambuyo pace, kuti awadzoze atazibvala, nadzaze manja ao atazibvala;

30. mwana wace wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwace azibvala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'cihema cokomanako kutumikira m'malo opatulika.

31. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nayama yace m'malo opatulika.

32. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mumtanga, pa khomo la cihema cokomanako.

33. Ndipo adye zimene anacita nazo coteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.

34. Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.

Eksodo 29