15. Ndipo uzipangira kacisi matabwa oimirika, a mtengo wasitimu.
16. Utali wace wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwace kwa thabwali mkono ndi hafu.
17. Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a kacisi.
18. Ndipo uzipanga matabwa a kacisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwela, kumwela.
19. Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri;
20. ndi pa mbali yace yina ya kacisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai;