9. Koma ngati amtomera mwana wace wamwamuna, amcitire monga kuyenera ana akazi.
10. Akamtengera mkazi wina, asacepetse cakudya cace, zobvala zace, ndi za ukwati zace zace.
11. Ndipo akapanda kumcitira izi zitatu, azituruka cabe, osaperekapo ndalama.
12. Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.
13. Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzace, ndidzakuikirani pothawirapo iye.