Eksodo 13:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo cizikhala ndi iwe ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi cikumbutso pakati pa maso ako; kuti cilamulo ca Yehova cikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakuturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.

10. Cifukwa cace uzikasunga lemba ili pa nyengo yace caka ndi caka.

11. Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,

12. kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.

13. Koma woyamba yense wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

Eksodo 13