17. Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati. Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kumka ku Aigupto.
18. Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kucipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israyeli anakwera kucokera m'dziko la Aigupto okonzeka.
19. Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israyeli ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawwya kuno.