Eksodo 12:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2. Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.

3. Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.

Eksodo 12