41. Pamenepo Mose anapatula midzi itatu tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;
42. kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:
43. ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.
44. Ndipo ici ndi cilamulo Mose anaciika pamaso pa ana a Israyeli;
45. izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israyeli, poturuka iwo m'Aigupto;
46. tsidya lija la Yordano, m'cigwa ca pandunji pa Beti Peori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israyeli anamkantha, poturuka iwo m'Aigupto;